01/04/2023
NO PAIN NO GAIN
💦💦💦💦💦💦💦💦💦💦💦💦💦💦💦💦💦💦💦💦💦💦💦💦💦💦💦
PART 22
✍️ BY MORGAN✍️
+265 88 499 55 66
Directed By Goshen.K
Sponsored By jacko mw
Search like and follow LIFE AND LOVE STORIE BY MORGAN for more.
Ndidaphitsa madzi otentha kwambili ndikuyamba kumuthowa Kaye miyendo paja idali itayamba kutupa before kumpatsa madzi osamba, zitatelo ndidakamuyikira madzi kubafa kuti akasambe moti momwe amkatuluka adandipeza nditapanga ka tea ndipo ataona izi adati...
""Moosah, ndikudziwa kuti unandikonda kwambili komanso umasamala za ine komabe on this moment sukuyenera kumandipangira zonsezi ayi chifukwa tili ndi zina zambili zoti tipange chifukwa ndi moyo omwe tayambawu ndikuyenera kudziwa kagwiridwe ka ntchito zosiyana siyana kuti mwina moyo usakhale olimba chifukwa mayi wangwiro amathandiza mwamuna wake kusaka ndalama munjira zina osati kumangodikira jumbo basi. Chimodzi modzinso bambo wangwiro amathandiza mkazi wake kugwira ntchito zina zapakhomo kupatula kusaka ndalamako zomwe zikuonetsa kuti ukukwanitsa ntchito yako ngati bambo wangwiro komabe ukuyenera kundiphumzitsa kugwira ntchito zina chifukwa ndimadziwa zochepa chabe kuti nane ndikhale bambo wangwiro""
Atalankhura mau awa ndidakhala pheee kumuyang'ana Nelli kenako ndidayamba kusekelera....
""Aaahh ndiye ukuseka?? Kusonyeza ndalankhula mbwerera kapena et?""
"" ainso koma basi zangondisangalatsa zomwe wanenazo maka maka zokuphumzitsa ntchitozo"".
""Aaahh nde uzindiseka??"".
"" vuto lokhala ana a adad ndi limeneli chifukwa ukanakhala wakumudzi bwemzitu ukudziwa chilichonse chomwe mkazi amayenera kuchita monga; kuchapa, kusinja, kupeta, kupita kuchigayo, kusinja, kutunga madzi, kuchapa, kuzira ndi zina koma kuti ndikufunse pamenepo kuti zomwe umadziwa kupanga ndichani mwinanso pa zomwe ndatchulazi sungatchule olo chimodzi,ndikunama???"".
""K*kk ukunama kumene, ndimadziwatu zinthu ine ngati kutunga madziko ndidatungapo tsiku lina kusukulu kwathu madzi atasiya ndiye ndizoti timayenera kutunga pa mjigo kuti tikasambe, pa nthawiyi kuwapempha azimzanga kuti anditungire aliyense amkandikanira chifukwa nawonso amkati kadali koyamba ndiye eeeeeh kudalitu zinthu. Tangoganiza mtsikana wamkulu kukanika kusemza madzi odzadza eti ? komabe ngakhale kadalo koyamba kwa ine ndidakwanitsa bwino bwino chifukwa sindimaziyang'anira pansi ayi mwanjira ina iam strong kungoona chinthu kamodzi ndimatha kupanga bwino bwinonso ngati momwe ochitayo anachitira.""
""Woow!!! Ok? ndiye ngati zili chomcho sizivuta chifukwatu nde msaname ndinali ndi nkhawa kuti nde tizipanga bwanji zinthu zinazi maka kuti ndikachokapo zizitani?"".
Tidapitiliza kucheza pamenepaja nkhani zingapo kenako ndidati....
""Honey, iyi ndi ndrama yokhayo yomwe ndatsala nayo ndiye ndimaona ngati titapangira ka business kena kake kuti mwina tithe kupanga survive bwino bwino, ukuona bwaz?"".
""Yaaa zoonadi sukunama dear, komano ndiye tipange business yanji kumudzi ngati kuno??"".
""Come on beb, kulikonsetu kuli ndalama chofunika ndikungopeza njira yopezera ndalamayo basi. I think udziphika kaya ndi mandasi udzigulitsa ineyo ndizisaka maganyu ena maka maka omangawa chifukwa kumanga nyumba ndimatha ndithu I think ndingotengapo ndrama iyi kuti ndikangopezako mpeni omangira ndi levulo chifukwa ndikuona ngati kumalo kunoko anthu akumanga manyumba ndithu akulu akulu olozeka ndiye siyingavute kupezeka ntchitoyo""...
""Ok ndizotheka komanso ndi plan yabwino, zitelo"".
""Komano iweyo ukwanitsa kuphika kwake kwa mandasiwo?""..
""Eya ndikwanitsa kwambilinso ndipo ngakhale kwathu ndimakonda kuphika ndine koma sindikudziwa ngati ndingakwanitse manual.""
Adalankhula Nelli zondilimbitsa mtima zija chifukwa ngakhale ndidanena za business iyiyi ngakhale ine sindimadziwa kuphika kwake.
""Ooh ok komano nthawi inayake ndikuyenera kukakuonetsa kumsika kuti kwina tikapeze malo ogulitsira komanso zina ndi zina"".
""Ok beb, komano ndiye akhale madzulo kuti ndizitolere pang'ono komanso ndikukhulupilira kuti sikutali eti??""..
Atalankhula chomchi ndidamuyang'ana kaye ndisadayankhe poti ndidadziwa pomwe padali nkhawa yake kenaka ndidamuyankha.
Titamaliza kukambilanaku ndidayamba zophika pakuti awano adali masana kotelo ndidamuitana Nelli kuti azionera chilichonse chomwe ndidzipanga ngati kumuphumzitsa chomcho chifukwa kwambili zomwe amatha iyeyo kudali kubeka zinthu ndi zina koma zophika msimazi nde sidali mbali yake .
Ndidamuphumzitsa zochepa zomwezo mpaka chakudya chidatheka ngakhale kuti nkhawa yanga idagonw poti mwina chakudyacho sachikonda kutengera ndikuti amzathu m'mipandamu amadalira kwambiri ma spice koma ndidadabwa momwe amadyera, zimkachita kuonetselatu kuti chakudyacho adachikonda ndithu.
Madzulo wa tsikuli tidanyamuka wakumsika kukamuonetsa malo angapo omwe amafunikira kwambiri kwa azimayi ngati kuchigayo mwa zina pakuti nane ndidali nditazunguliramo kale monsemu maka munthawi yomwe ndimakasaka nyumba ija mchifukwa chake ndimaonekako ngati shasha kenako tidapita ku msika kuja ndipo
titamaliza zonse tidagula zofunikira zonse kenako tidabwerera ulendo wakunyumba, titafika tidaphika mkudya kenako tidagona..
Ma'mawa kutacha ndidalawilira kumudzutsa Nellie kuti apange zophika mandasi chifukwa adali atapanga zofunikira zonse, atadzuka' tidathandizana kupanga ziwili zitatu mpaka momwe dzuwa lidatuluka, ndidamutsamzika kuti nane ndikayambepo kusaka kenako ndidanyamuka kumusiya iye atatsala pang'ono kumaliza...
Ndidayenda malo angapo kusakasaka koma ndikudutsa malo ena ndidamva kuitana cha kumbuyo kwanga....
""Malume!!!!!! Malume...... Inu mwanyamula levulonu tabwerani!!!!!!!"".
Nditamva zoti atchula za levulo ndidacheuka kenako ndidaona mzibambo wina akundikodora.Mosazengereza ndidanyamukadi mkupita ndipo nditafika adanditengera ku mpanda wina ndipo mosakhalitsa ndidaona bambo wina akutuluka mnyumbamu ndipo adati....
""Mwadzuka bwanji akulu""
""Ndadzuka bwino kaya inu bwana"".
""Inenso ndadzuka bwino, ok ndikhululupilira kuti mumadziwa kumanga bwino lomwe sichomcho??""
""Kwambili bwana, ndimadziwa ndithu ndipo imeneyo ndiyo ntchito yanga"".
Ndidayankha mopanda mantha kapena nkhawa pasi pa mtima ndikusangalala kuti yehova wayankha pemphero langa koma mbali inainso ndikurabashika malilime kuti bola zitheke.
""Ooh ok, choyamba ndikudziwitseni kuti pano pafika azimisili angapo ndithu koma onsewo sakhalitsapo chifukwa cha kusatha kugwira bwino ntchito komanso kuba simenti mwa zina, ndiye ndisadakupatseni chochita ndikufuna mungotipangira kachimbuzi ka panja kuseliku kuti tione momwe mumagwilira ntchito mwina ngati mungachite mwayi ndipomwe tingaone kuti titani...""
"" chabwino bwana"".
Ndidanyamukadi ulendo wa kuseri. Ndidasonkganitsa zida zonse zofunikira kenako ndidayambapo kugwira ntchito ndiye poti ndidayamba molawilirako' m'mene imati 4:30 ndidali ndikumaliza..
Nditamaliza ndidadzikomzekeletsa bwino kenakeno bwana adabwera kudzaona momwe ndidagwilira.
""Ooohh, mukuoneka kuti muli ndi lusotu malume, mwamanga bwino kwambili ndipo chikuchita kuoneka bwino msaname, apapa nde ndapezano m'misili odziwa sure"".
Adatelotu bwanawa pondiyamikira, kenaka adapitiliza kulankhulako.
""Now poti kwada kale apa chomwe tingachite mawa mudzayesetse muzabwere mwachangu kwambili chifukwa ndikufuna ndikakuonetseni malo oti muzikagwira ntchito koma mudzafike ngati m'misiritu, I mean mudzatenge zida zanu zonse zogwilira ntchito kuphatikizapo chingwe ndi square""..
Atalankhula izi ndidazimvera chisoni ndipo nawo mantha adayamba kundikwawira poganizira kuti zinthu zikunenedwazo ndilibe komanso kuti ngati ndingawauze chilungamo mwina atha kundikaikira kuti sine okwanira ngakhale kuti akadatelo akadakhala akukaikira zoona chifukwa umisiri ndimaudziwa ndithu kamba kokhala kumudzi komano sindimautenga ngati ingakhale ntchito yanga, kotelo ndidalibe zida zondiyenereza kukhala m'misiri weni weni koma ngakhale izi zidali chomcho, ndidasankhabe kunena chilungamo pozindikira kuti nthawi zina chilungamo chikagwilitsidwa bwino ntchito chimathandiza.
""Ooohh yaap ndikadakonda ndikadatelo koma vuto zida zina ndilibe ndiye sindikudziwa kuti pamenepo tidzapanga bwanji koma ntchitoyo ndikuifuna ndithu""
Nditalankhula mau awa bwanawa adandiyang'ana mwa chidwi kwambiri zomwe zidatsetsa mantha akulu mu mtima mwanga, koma adati..
""Aaah mzotelonso kani, ok basi zabwereni poti mkuyamba kukuonani bwezi nditakupatsani ndrama kuti mukagule chikhala tikudziwana bwino lomwe koma apopo ndiye kuti tidzangopitira limodzi kokagulako basi. Kumbali ya ntchito yomwe mwagwirayi nde sindikudziwa kuti mundipanga ndrama zingati""
""Aahh bwana msaname ndangobwera kumene ine kuno ndiye momwe zinthu zimakhalira sindikudziwa bwino bwino, tangondipatsani yomwe mungaoneyo basi poti tidakali limodzi""..
""Malume, mukupangaotu ndi malonda a mphaka, Mesa ntchito mwagwira ndi inu ndiye mukufuna nditchaje ine zoona??.."".
""Not kutchaja as such komano poti sindikudziwa momwe zinthu kunoko zimakhalira ndiye kwalelolo mungopanga mulimonsemo basi komano ndikafufuza momwe zimakhalira ndiye kuti ndizikuwuzani ntchito zina zikamapezeka komano apapa titelo ndithu bwana wanga.""
""Okay, sikuti sindimadziwatu ayi komano ndimangofuna ndimve kumbali yanu chifukwa ntchitoyi mwaigwiranso mwachangu, mwanjira ina nditha kunena kuti mtengo wa pa day ndi 3000 m'misili komano inuyo ndikupatseni 8000 sinanga mumadzipatsiranso nokha matope komanso chifukwa chogwira bwino ntchito ndionjezerapo 1000 ngati 9000 pamodzi , eni iyi....""
Ndidalandira ndrama ija kenako ndidatsamzika wakunyumba, nditafika ndidapeza Nelli atafika kale....
""Welcome back home honey"".
Adatelo atangondiona uku akubwera kudzandihaga...
""Thanks beb""...
Ndidatelo uku tikuhagana kenako adalandira jumbo yomwe ndidanyamura mkundigwira mchiuno ulendo wa mnyumba....
Nditangokhala pang'ono mnyumba muja anakandisiyira madzi kenako ndidapita kukasamba, nditamaliza ndidamupeza akupanga za chakudya ...
""Hey, mukufuna muphikeno??"".
""Yap inuyo pheee muone zomwe ndingakupangireni ""
"" woow, ok will be waiting patiently""..
""Ok you are welcome""
Amayankhatu uku ali busy namwaliyu kugwira gwira za pamoto, ine ndimangomuyang'ana pheeee....
Atamaliza adabweretsa chilichonse pa phasa pomwe ndidakhalapo kenako naye adabwera pomwepo ndikudzakhala pansi kenako adati....
""Beb ulaweko ntchito za manja anga tsopano ""
Adalankhula uku alumwetulira, zitatelo adapemphera kenako tidayamba kudya koma kunena monenetsa adaphika bwino koposa moti zoti ndiwo zake zidali (soya pieces or soya meat) kuletsa ndithu...
Tidadya pamenepaja ndipo ndidayamikira kwambili maka momwe adaphikira mpaka ndidafunsa yemwe adamuwuza za kaphikidwe ka bowayu koma adandibisira....
""Beb, tizibisirana zinthu et?""
Ndidalankhula mowonetsa nkhope yokhumudwa dala dala ndicholinga choti andiuze mpaka adandiuzadi.
""Basi mtima wakhalano pansi eti?""
""K*k yah bola pamenepo chifukwa ukadangondibisira ndikadakwiyatu ohooo"".
""aahh nkhani yake itiyo komanso bolanso ndikadapanda kukuwuzatu ""
""Munthu oti wandiuza kale ... Apapa ndakuwina vomelezani basi"" .
""Ok wawinadi tidzaona tsiku lina. eeehh komadi kodi kuntchito mwayendako bwanji??
""Aahhh himm koma zoona monse muja udzikafunsa pano??"".
""Aahh Mesa iweyo...
""Ineyo ndatani?""..
""Umandibalalitsa kaya ndipo sindimamvetsa kuti udanditani msaname eeee, ndimangodzimva kutsekemera paliponse ndikakhala nawe, i think iam just a little crazy.""
""K*k ukadadziwa momwe ndimamvera za iwe sukadanena, taganiza ngati ndidafika pololera izizi do u think it's a jock??"".
""Unene ineyo , ngati ndidalolera izizi do you think ndi nthabwala??""..
""Eeeesh basi tisakangane apa nkhani ndi ya straight, we love each other equally"".
""K*kk yaaaa""
Ndidacheza nkhani zosiyana siyana pamenepaja kuphatikizapo kuwuzana momwe aliyense wayendera kumandala (kosaka ndalama) kenako tidagona.
Ma'mawa kutacha tidachitanso chimodzi modzi monga tidachitira dzulo lake. kenako ndidanyamuka molawira kwambili kutengela ndi zomwe tidagwilizana ndi bwana aja ndipo nditafika ndidawapeza ndithu akutuluka mnyumba komanso adali atakomzeka ndithu, mosataya nthawi tidanyamuka ulendo wa ku plot yawo ina yomwe amkafunako kumanga nyumba, kenako tidanyamuka wa mtown kukagula zinthu zogwilira ntchito. tili mu shop momwemo ndidakumana ndi........
Nkhaniyi ikupitilira.....
comment and share kuti part ina ikufikeni mwa msanga....
Ndimakunyadirani nonse
👏👏👏👏👏👏👏👏👏👏👏👏👏
Tikumane mu part ina